Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 4

Yesu Aletsa Namondwe

35 Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, "Tiyeni tiwolokere tsidya lina." 36 Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye. 37 Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. 38 Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, "Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?"

39 Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, "Chete! Khala bata!" Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.

40 Iye anati kwa ophunzira ake, "Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?"

41 Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, "Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!"

Veja também