Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 4

37 Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. 38 Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, "Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?"

39 Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, "Chete! Khala bata!" Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.

40 Iye anati kwa ophunzira ake, "Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?"

41 Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, "Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!"

Veja também