38 Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, "Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?"
39 Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, "Chete! Khala bata!" Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.
40 Iye anati kwa ophunzira ake, "Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?"