22 mmodzi wa akulu a mʼsunagoge, dzina lake Yairo anafika pamenepo. Ataona Yesu, anagwa pa mapazi ake, 23 ndi kumudandaulira kwambiri nati, "Mwana wanga wamkazi wamngʼono ali pafupi kufa. Chonde tiyeni kuti mukamusanjike manja kuti akachiritsidwe nakhala ndi moyo." 24 Ndipo Yesu anapita naye.
Gulu lalikulu la anthu linamutsata ndi kumamupanikiza Iye.