Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 5

25 Pomwepo panali mayi amene amadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri. 26 Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe. 27 Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake, 28 chifukwa anaganiza kuti, "Ngati nditangokhudza mkanjo wake, ndidzachiritsidwa." 29 Nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka ndipo anamva mʼthupi mwake kuti wamasulidwa ku vuto lake.

30 Pomwepo Yesu anazindikira kuti mphamvu inachoka mʼthupi mwake. Anatembenuka mʼgulu la anthu ndipo anafunsa kuti, "Ndani wakhudza zovala zanga?"

31 Ophunzira ake anayankha kuti, "Mukuona kuti anthu akukupanikizani, ndipo Inu mukufunsa kuti, Ndani wandikhudza?’ "

32 Koma Yesu anapitirizabe kuyangʼana kuti aone amene anachita zimenezi. 33 Kenaka mayi uja pozindikira chimene chinamuchitikira, anabwera ndi kugwa pa mapazi ake, ndipo akunjenjemera ndi mantha, anamuwuza zoona zokhazokha. 34 Anati kwa iye, "Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere ndipo khala womasulidwa ku mavuto ako."

Veja também