Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 5

38 Atafika ku nyumba ya mkulu wa sunagoge, Yesu anaona chipiringu cha anthu akulira ndi kufuwula kwambiri. 39 Analowa nati kwa iwo, "Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo." 40 Koma anamuseka Iye.

Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo. 41 Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, "Talita Kumi!" (Kutanthauza kuti, "Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!") 42 Nthawi yomweyo anayimirira nayenda mozungulira (anali wa zaka khumi ndi ziwiri). Pa ichi onse anadabwa kwambiri.

Veja também