22 Mwana wamkazi wa Herodia atabwera ndi kudzavina, anakondweretsa Herode ndi alendo ake a pa mphwandopo.
Mfumu inati kwa mtsikanayo, "Undipemphe chilichonse chimene ukuchifuna, ndipo ndidzakupatsa." 23 Ndipo analonjeza ndi lumbiriro kuti, "Chilichonse chimene upempha ndidzakupatsa, ngakhale theka la ufumu wanga."
24 Iye anatuluka nati kwa amayi ake, "Kodi ndikapemphe chiyani?"
Iye anamuyankha kuti, "Mutu wa Yohane Mʼbatizi."
25 Nthawi yomweyo mtsikana uja anafulumira kupita komwe kunali mfumu ndi pempho lake: "Ndikufuna kuti mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale."
26 Mfumu inamva chisoni chachikulu, koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo ake a pa mphwandolo, sanafune kumukaniza. 27 Nthawi yomweyo iye anatumiza yemwe anali ndi ulamuliro wonyonga anthu kuti abweretse mutu wa Yohane. Munthuyo anapita, nakadula mutu wa Yohane mʼndende, 28 nabweretsa mutuwo mʼmbale. Anawupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anakapereka kwa amayi ake.