35 Pa nthawi iyi nʼkuti dzuwa litapendeka, ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye nati, "Kuno ndi kuthengo, ndipo ano ndi madzulo. 36 Awuzeni anthuwa azipita ku midzi ndi madera ozungulira, kuti akadzigulire kanthu kakuti adye."
37 Koma Iye anayankha kuti, "Apatseni kanthu koti adye."
Iwo anati kwa Iye, "Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?"
38 Iye anawafunsa kuti, "Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone."
Ataona anati kwa Iye, "Asanu ndi nsomba ziwiri."
39 Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. 40 Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. 41 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. 42 Onse anadya ndipo anakhuta, 43 ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri. 44 Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000.