Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 7

11 Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani(kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), 12 pamenepo inu simumalola kuti achitire kanthu kalikonse abambo kapena amayi ake. 13 Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi."

14 Yesu anayitananso gulu la anthu ndipo anati, "Tandimverani nonsenu, ndipo zindikirani izi. 15 Palibe kanthu kunja kwa munthu kamene kakalowa mwa iye kangamusandutse wodetsedwa. Koma zimene zituluka mwa munthu ndizo zimupanga kukhala wodetsedwa."

Veja também