Chikhulupiriro cha Mayi wa ku Siriya Fonisia
24 Yesu anachoka kumalo amenewo napita ku madera a Turo. Iye analowa mʼnyumba ndipo sanafune wina kuti adziwe zimenezi; komabe sanathe kudzibisa. 25 Kunena zoona, amayi amene kamwana kawo kakakazi kanali kogwidwa ndi mzimu woyipa, atangomva za Iye, anabwera nagwada pa mapazi ake. 26 Mayiyu anali Mhelene, wobadwira ku Fonisia wa ku Siriya. Anamupempha Yesu kuti atulutse chiwanda mwa mwana wake.
27 Iye anamuwuza kuti, "Choyamba asiye ana adye zimene akuzifuna, pakuti si kwabwino kutenga buledi wa ana ndi kuponyera agalu awo."
28 Mayiyo anayankha kuti, "Inde Ambuye, koma ngakhale agalu amadya zomwe zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la ana."
29 Ndipo Iye anamuwuza kuti, "Chifukwa cha yankholi, ukhoza kupita; chiwanda chachoka mwa mwana wako wamkazi."
30 Atapita kwawo anakapeza mwana wake aligone pa bedi, chiwanda chitatuluka.