Pular para o conteúdo
Publicidade

MARKO 7

9 Ndipo anawawuzanso kuti, "Inu muli ndi njira yabwino yokankhira kumbali malamulo a Mulungu kuti mukatsatire miyambo yanuyo! 10 Pakuti Mose anati, Lemekeza abambo ako ndi amayi ako,ndipo, aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. 11 Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani(kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), 12 pamenepo inu simumalola kuti achitire kanthu kalikonse abambo kapena amayi ake. 13 Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi."

Veja também