Yesu Adyetsa Anthu 4,000
1 Mʼmasiku amenewo gulu lina lalikulu la anthu linasonkhana. Popeza iwo analibe chakudya, Yesu anayitana ophunzira ake nati kwa iwo, 2 "Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala ali ndi Ine masiku atatuwa ndipo alibe chakudya. 3 Ngati nditawawuza kuti apite kwawo ali ndi njala, iwo adzakomoka mʼnjira chifukwa ena a iwo achokera kutali."
4 Ophunzira ake anayankha nati, "Kodi ndi kuti kuthengo kuno kumene munthu angapeze buledi okwanira kuwadyetsa?"
5 Yesu anafunsa kuti, "Muli ndi malofu a buledi angati?"
Iwo anayankha kuti, "Asanu ndi awiri."
6 Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero. 7 Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. 8 Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. 9 Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo,