Pular para o conteúdo
Publicidade

MARKO 8

Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosaona ku Betisaida

22 Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze. 23 Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, "Kodi ukuona kalikonse?"

24 Iye anakweza maso nati, "Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda."

25 Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino. 26 Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, "Usapite mʼmudzimo."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também