Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 9

17 Munthu wina mʼgululo anayankha kuti, "Aphunzitsi, ndinakubweretserani mwana wanga wamwamuna, amene ndi ogwidwa ndi mzimu umene umamulepheretsa kuyankhula. 18 Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe."

19 Yesu anayankha kuti, "Haa! Mʼbado osakhulupirira, kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Mubweretseni kwa Ine mnyamatayo."

20 Ndipo anamubweretsa kwa Iye. Mzimu woyipawo utaona Yesu, nthawi yomweyo unamukomola mnyamatayo. Anagwa pansi ndi kumagubuduka, ndi kuchita thovu kukamwa.

21 Yesu anafunsa abambo a mnyamatayo kuti, "Kodi wakhala chotere nthawi yayitali bwanji?"

Iye anayankha kuti, "Kuyambira ali wamngʼono, 22 wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize."

23 Yesu anati, " Ngati mungathe!Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira."

24 Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, "Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!"

25 Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti, "Iwe mzimu wolepheretsa kuyankhula ndi kumva, ndikulamulira tuluka mwa iye ndipo usadzalowenso."

26 Mzimuwo unafuwula ndi kumugubuduza kwambiri ndipo unatuluka. Mnyamatayo anaoneka ngati mtembo ndipo ambiri anati, "Wafa." 27 Koma Yesu anamugwira dzanja ndipo anamuyimiritsa, ndipo anayimirira.

Veja também