8 "Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera.
"Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’
"Pa zakhumi ndi pa zopereka. 9 Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. 10 Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga." Akutero Yehova Wamphamvuzonse, "Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo.