Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 1

Kubadwa kwa Yesu Khristu

18 Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. 19 Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.

20 Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, "Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. 21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo."

Veja também