Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 1

20 Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, "Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. 21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo."

22 Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, 23 "Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli," kutanthauza kuti, "Mulungu ali nafe."

24 Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake. 25 Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.

Veja também