Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 11

Tsoka la Mizinda Itatu Yosatembenuka mtima

20 Pamenepo Yesu anayamba kudzudzula mizinda imene zodabwitsa zake zambiri zinachitikamo, chifukwa chakuti sinatembenuke mtima. 21 "Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betisaida! Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe zikanachitidwa mu Turo ndi Sidoni, iwo akanalapa kale atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 22 Koma ndikuwuzani inu kuti pa tsiku lachiweruzo mlandu wa Turo ndi Sidoni udzachepako kusiyana ndi wanu. 23 Ndipo iwe Kaperenawo, kodi udzakwezedwa kufika kumwamba? Ayi, udzatsitsidwa mpaka pansi kufika ku Hade. Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe, zikanachitika mu Sodomu, bwenzi iye alipo kufikira lero. 24 Koma Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro mlandu wa Sodomu udzachepako kusiyana ndi wanu."

Veja também