Amayi ndi Abale Ake a Yesu
46 Pamene Yesu anali kuyankhulabe ndi gulu la anthu, amayi ndi abale ake anayimirira kunja, akufuna kuyankhulana naye. 47 Wina anamuwuza Iye kuti, "Amayi ndi abale anu ayima kunjaku akufuna kuyankhulana nanu."
48 Iye anayankha kuti, "Amayi anga ndani ndipo abale anga ndi ndani?" 49 Ndipo akuloza ophunzira ake, Iye anati, "Awa ndiwo amayi anga ndi abale anga. 50 Pakuti aliyense amene achita chifuniro cha Atate anga akumwamba ndiye mʼbale wanga, mlongo wanga ndi amayi anga."