14 Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa:
" ‘Kumva mudzamva koma osamvetsetsa.
Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu.
15 Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika,
mʼmakutu mwawo ndi mogontha,
ndipo atsinzina
kuti asaone kanthu.
Mwina angapenye ndi maso awo,
angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,
Ineyo nʼkuwachiritsa.’