Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 13

14 Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa:

" Kumva mudzamva koma osamvetsetsa.

Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu.

15 Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika,

mʼmakutu mwawo ndi mogontha,

ndipo atsinzina

kuti asaone kanthu.

Mwina angapenye ndi maso awo,

angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,

Ineyo nʼkuwachiritsa.

16 Koma maso anu ndi odala chifukwa amapenya ndi makutu anu chifukwa amamva.

Veja também