Publicidade

Mateus 13

Fanizo la Namsongole

24 Yesu anawawuza fanizo lina kuti: "Ufumu wakumwamba ufanana ndi munthu amene anafesa mbewu zabwino mʼmunda mwake. 25 Koma aliyense akugona usiku mdani wake anabwera ndi kufesa namsongole pakati pa tirigu ndipo anachoka. 26 Pamene tirigu anamera ndi kutulutsa ngala, namsongole anaonekanso.

27 "Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?

28 "Iye anayankha kuti, Ndi mdani amene anachita izi.

"Antchito anamufunsa iye kuti, Kodi mufuna kuti tipite tikamuzule?

29 "Iye anakana nati, Ayi. Chifukwa pamene mukuzula namsongoleyo mwina inu mungazulire pamodzi ndi tirigu. 30 Zisiyeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Pa nthawi imeneyo ndidzawuza okolola kuti: Poyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga mʼmitolo kuti atenthedwe, kenaka sonkhanitsani tirigu ndi kumuyika mʼnkhokwe yanga.’ "

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-28_14-13-17-