Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 13

3 Pamenepo Iye anawawuza zinthu zambiri mʼmafanizo ndi kuti, "Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. 4 Akufesa, zina zinagwera mʼmbali mwa njira ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. 5 Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. 6 Koma dzuwa litakwera, mbewu zinapserera ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. 7 Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. 8 Koma mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala zipatso 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa. 9 Amene ali ndi makutu amve."

Veja também