15 Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, "Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya."
16 Yesu anawayankha kuti, "Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye."
17 Iwo anayankha kuti, "Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri."
18 Koma Iye anati, "Bweretsani kwa Ine." 19 Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu. 20 Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri. 21 Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.