Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 15

Mayi wa ku Kanaani

21 Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni. 22 Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, "Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda."

23 Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, "Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu."

24 Iye anayankha kuti, "Ine ndinatumidwa kwa nkhosa zotayika za Israeli zokha."

25 Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, "Ambuye ndithandizeni!"

26 Iye anayankha kuti, "Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu."

27 Mayiyo anati, "Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo."

28 Pomwepo Yesu anayankha kuti, "Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka." Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.

Veja também