32 Yesu anayitana ophunzira ake nati, "Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala kale ndi Ine masiku atatu ndipo alibe chakudya. Ine sindifuna kuti apite kwawo ndi njala chifukwa angakomoke pa njira."
33 Ophunzira anayankha kuti, "Ndikuti kumene tingakapeze buledi mʼtchire muno okwanira kudyetsa gulu lotere?"
34 Yesu anawafunsa kuti, "Muli ndi malofu a buledi angati?"
Iwo anayankha kuti, "Asanu ndi awiri ndi tinsomba pangʼono."
35 Iye anawuza gululo kuti likhale pansi. 36 Kenaka anatenga malofu asanu ndi awiri aja ndi tinsombato ndipo atayamika anagawa napatsa ophunzira ake ndipo iwo anagawira anthuwo. 37 Onse anadya ndipo anakhuta. Pomaliza ophunzira anatolera zotsalira nadzaza madengu asanu ndi awiri. 38 Chiwerengero cha anthu amene anadya chinali 4,000 kupatula amayi ndi ana.