Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 16

Yisiti wa Afarisi ndi Asaduki

5 Koma atawoloka nyanja, ophunzira anayiwala kutenga buledi. 6 Yesu anawawuza kuti, "Chenjerani, khalani tcheru ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki."

7 Iwo anakambirana pakati pawo za izi ndipo anati, "Ichi nʼchifukwa chakuti sitinatenge buledi aliyense."

8 Yesu atadziwa zokambirana zawo, anawafunsa kuti, "Chifukwa chiyani mukukambirana zakuti, mulibe buledi?Inu achikhulupiriro chochepa. 9 Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza? 10 Kapena buledi musanu ndi muwiri amene anadya anthu 4,000, nanga ndi madengu angati amene munadzaza? 11 Zitheka bwanji kuti inu simukumvetsetsa kuti Ine sindinkayankhula nanu za buledi? Koma inu chenjerani ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki." 12 Kenaka iwo anazindikira kuti Iye samawawuza kuti achenjere ndi yisiti wa buledi koma ndi chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.

Veja também