Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 17

Yesu Apereka Msonkho

24 Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, "Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?"

25 Iye anayankha kuti, "Inde amapereka."

Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, "Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?"

26 Petro anayankha kuti, "Kuchokera kwa ena."

Yesu ananena kwa iye kuti, "Ndiye kuti ana sapereka." 27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.

Veja também