Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 18

Za Mʼbale Amene Akuchimwirani

15 "Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo. 16 Koma ngati sakumvera, katenge wina mmodzi kapena ena awiri, kuti nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu. 17 Ngati iye akana kuwamvera iwo, kaneneni ku mpingo; ndipo ngati sakamvera ngakhale mpingo, muchite naye monga mukanachitira ndi wakunja kapena wolandira msonkho.

18 "Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba.

19 "Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani. 20 Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo."

Veja também