23 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, "Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. 24 Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu."
25 Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, "Nanga angapulumuke ndani?"
26 Yesu anawayangʼana iwo nati, "Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka."