Anzeru a Kummawa
1 Atabadwa Yesu mʼBetelehemu wa ku Yudeya, mʼnthawi ya mfumu Herode, Anzeru a kummawa anabwera ku Yerusalemu 2 nafunsa kuti, "Ali kuti amene wabadwa kukhala mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kummawa ndipo tabwera kudzamupembedza."
3 Mfumu Herode atamva zimenezi, anavutika mu mtima kwambiri pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu. 4 Ndipo anayitanitsa anthu onse, akulu ansembe ndi aphunzitsi amalamulo nawafunsa kuti, "Kodi Khristu adzabadwira kuti?" 5 Ndipo anamuyankha kuti, "Ku Betelehemu wa ku Yudeya chifukwa izi ndi zimene mneneri analemba kuti,
6 " ‘Koma iwe Betelehemu, chigawo cha Yudeya,
sindiwe wamngʼonongʼono mwa olamulira a Yudeya;
pakuti otsogolera adzachokera mwa iwe,
amene adzaweta anthu anga Aisraeli.’ "
7 Pomwepo Herode anawayitanira mseri Anzeruwo nawafunsitsa nthawi yeniyeni yomwe nyenyeziyo inaoneka. 8 Ndipo anawatumiza ku Betelehemu nawawuza kuti, "Pitani mukafufuze za mwanayo mosamalitsa. Ndipo mukamupeza mudzandiwuze kuti inenso ndikamupembedze."
9 Atamva mawu a mfumu, ananyamuka ulendo wawo, ndipo taonani nyenyezi anayiona kummawa ija, inawatsogolera mpaka inayima pamwamba pa nyumba yomwe munali mwanayo. 10 Pamene iwo anaona nyenyeziyo, anasangalala kwambiri. 11 Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira Iye. Pomwepo anamasula chuma chawo ndi kupereka mphatso zawo za ndalama zagolide, lubani ndi mure. 12 Ndipo atachenjezedwa mʼmaloto kuti asapitenso kwa Herode, anabwerera ku dziko la kwawo podzera njira ina.