Pular para o conteúdo
Publicidade

MATEYU 20

Yesu Achiritsa Anthu Awiri Osaona

29 Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata. 30 Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, "Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!"

31 Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, "Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!"

32 Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, "Mukufuna ndikuchitireni chiyani?"

33 Anamuyankha nati, "Ambuye, tikufuna tione!"

34 Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também