Yesu Atemberera Mtengo wa Mkuyu
18 Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala. 19 Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, "Usadzabalenso chipatso!" Nthawi yomweyo mtengowo unafota.
20 Ophunzira ataona zimenezi, anadabwa nafunsa kuti, "Kodi mtengo wamkuyuwu wauma msanga bwanji?"
21 Yesu anayankha kuti, "Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi. 22 Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero."