Pular para o conteúdo
Publicidade

MATEYU 22

Ukwati ndi za Kuuka kwa Akufa

23 Tsiku lomwelo Asaduki amene amati kulibe za kuukanso, anabwera kwa Iye ndi funso. 24 Iwo anati, "Aphunzitsi, Mose anatiwuza kuti munthu akamwalira wosasiya ana, mʼbale wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 25 Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo. 26 Izi zinachitikiranso mʼbale wa chiwiri ndi wachitatu mpaka wachisanu ndi chiwiri. 27 Pa mapeto pake mkaziyo anamwaliranso. 28 Tsopano, kodi akadzaukitsidwa adzakhala mkazi wa ndani mwa asanu ndi awiriwa popeza aliyense anamukwatirapo?"

29 Yesu anayankha kuti, "Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu. 30 Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 31 Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti, 32 Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo."

33 Magulu a anthu atamva zimenezi, anazizwa ndi chiphunzitso chake.

Veja também