29 "Akadzangotha mavuto a masiku amenewo,
" ‘dzuwa lidzadetsedwa,
ndipo mwezi sudzawala;
nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba,
ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.’
30 "Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu. 31 Ndipo adzatuma angelo ake, ndi kulira kwa lipenga kwakukulu, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinayi, ndi kuchokera kumathero a thambo kufika mbali ina.