Pular para o conteúdo
Publicidade

MATEYU 24

Wantchito Wokhulupirika ndi Wosakhulupirika

45 "Kodi wantchito wokhulupirika ndi wanzeru amene ambuye ake anamuyika kukhala woyangʼanira antchito a mʼnyumba kuti awapatse chakudya chawo pa nthawi yake ndani? 46 Chidzakhala chabwino kwa wantchitoyo ngati mbuye wake pofika adzamupeza akuchita zimenezi. 47 Zoonadi, ndikuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense. 48 Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo ndi woyipa, nati kwa iye yekha, Mbuye wanga akuchedwa kubwera, 49 nayamba kumenya antchito anzake, nadya ndi kumwa ndi zidakwa. 50 Mbuye wa wantchitoyo adzabwera pa tsiku limene iye samamuyembekezera ndi pa nthawi imene iye sakuyidziwa. 51 Adzamulanga koopsa ndipo adzamuyika kokhala anthu achiphamaso, kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também