3 Yudasi, amene anamupereka Iye, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti akaphedwe, anatsutsika mu mtima mwake nakabweza ndalama zamasiliva makumi atatu zija kwa akulu a ansembe ndi kwa akuluakulu. 4 Iye anati, "Ndachimwa pakuti ndapereka munthu wosalakwa."
Iwo anayankha nati, "Ife tilibe nazo kanthu izo ndi zako."
5 Pamenepo Yudasi anaponya ndalamazo mʼNyumba ya Mulungu nachoka. Kenaka anapita nakadzimangirira.