Yohane Mʼbatizi
1 Mʼmasiku amenewo, Yohane Mʼbatizi anadza nalalikira mʼchipululu cha Yudeya 2 kuti, "Tembenukani mtima chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira." 3 Uyu ndi amene mneneri Yesaya ananena za iye kuti,
"Mawu a wofuwula mʼchipululu,
‘Konzani njira ya Ambuye,
wongolani njira zake.’ "
4 Zovala za Yohane zinali zopangidwa ndi ubweya wa ngamira, ndipo amamangira lamba wachikopa mʼchiwuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wa kuthengo. 5 Anthu ankapita kwa iye kuchokera ku Yerusalemu ndi ku Yudeya konse ndi ku madera onse a Yorodani. 6 Ndipo akavomereza machimo awo ankabatizidwa mu mtsinje wa Yorodani.