Yesu Ayesedwa Mʼchipululu
1 Pambuyo pake Yesu anatsogozedwa ndi Mzimu Woyera kupita ku chipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. 2 Ndipo atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, anamva njala. 3 Woyesayo anadza kwa Iye nati, "Ngati ndinu mwana wa Mulungu, sandutsani miyala iyi kuti ikhale buledi."
4 Yesu anayankha kuti, "Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ "
5 Pamenepo mdierekezi anapita naye ku mzinda woyera namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. 6 Ndipo anati, "Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa:
" ‘Adzalamulira angelo ake za iwe,
ndipo adzakunyamula ndi manja awo
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ "
7 Yesu anamuyankha kuti, "Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ "
8 Kenaka mdierekezi anamutengera Yesu ku phiri lalitali kwambiri namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo. 9 Ndipo anati kwa Iye, "Zonsezi ndidzakupatsani ngati mutandiweramira ndi kundipembedza ine."
10 Yesu anati kwa iye, "Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ "
11 Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye.