Pular para o conteúdo
Publicidade

MATEYU 4

Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba

18 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi. 19 Yesu anati, "Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu." 20 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.

21 Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana. 22 Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.

Veja também