Zopereka Zachifundo
1 "Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba.
2 "Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse. 3 Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita, 4 kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho.
6 Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho.