Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateyu 6:5-15

Za Kupemphera

5 "Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 6 Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho. 7 Ndipo pamene mukupemphera, musamabwerezabwereza monga akunja, pakuti iwo amaganiza kuti adzamveka chifukwa chochulutsa mawu. 8 Musakhale ngati iwo chifukwa Atate anu amadziwa zimene musowa musanapemphe.

9 "Chifukwa chake pempherani motere:

" ‘Atate athu akumwamba,

dzina lanu lilemekezedwe,

10 Ufumu wanu ubwere,

chifuniro chanu chichitike

pansi pano monga kumwamba.

11 Mutipatse chakudya chathu chalero.

12 Mutikhululukire mangawa athu,

monga ifenso tawakhululukira amangawa athu.

13 Ndipo musatitengere kokatiyesa;

koma mutipulumutse kwa woyipayo.’

14 Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani. 15 Koma ngati inu simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.