Pular para o conteúdo
Publicidade

MATEYU 8

Yesu Aletsa Namondwe

23 Iye atalowa mʼbwato, ophunzira ake anamutsatira. 24 Ndipo taonani mwadzidzidzi mphepo yayikulu yamkuntho inawomba pa nyanjapo, kotero kuti bwatolo linayamba kumizidwa ndi mafunde. Koma Yesu anali mtulo. 25 Ophunzira ake anapita namudzutsa nati, "Ambuye! Tipulumutseni! Tikumira!"

26 Iye anawayankha kuti, "Inu achikhulupiriro chochepa, chifukwa chiyani mukuchita mantha?" Ndipo anayimirira nadzudzula mphepoyo ndi mafunde ndipo panali bata lalikulu.

27 Ndipo ophunzirawo anadabwa nafunsa kuti, "Ndi munthu wotani uyu? Kuti ngakhale mphepo ndi mafunde zimvera Iye!"

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também