Ogwidwa ndi Ziwanda a ku Gadara
28 Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo. 29 Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, "Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?"
30 Ndipo patali pake panali gulu la nkhumba zimene zimadya. 31 Ndipo ziwandazo zinamupempha Yesu kuti, "Ngati mutitulutsa ife mutitumize mu nkhumba izo."
32 Iye anati kwa ziwandazo, "Pitani!" Ndipo pamenepo zinatuluka ndi kukalowa mʼnkhumbazo ndipo nkhumba zonse zinathamangira mʼnyanja ndi kufera momwemo. 33 Koma amene amaziweta anathawa nalowa mʼmudzi nafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitika ndi anthu ogwidwa ndi ziwanda aja. 34 Ndipo anthu onse a mʼmudziwo anatuluka kukakumana ndi Yesu. Ndipo atamuona Iye, anamupempha kuti achoke mʼdera lawo.