Pular para o conteúdo
Publicidade

MATEYU 9

Za Mwana Wamkazi wa Yairo ndi Mayi Wokhudza Chovala cha Yesu

18 Pamene ankanena zimenezi, mkulu wa sunagoge anabwera namugwadira Iye nati, "Mwana wanga wamkazi wamwalira posachedwapa koma tiyeni mukasanjike dzanja lanu pa iye ndipo adzakhala ndi moyo." 19 Yesu ndi ophunzira ake ananyamuka napita naye pamodzi.

20 Panali mayi wina amene ankadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri ndipo anadza mʼmbuyo mwake nakhudza mkanjo wake. 21 Iyeyo anati mwa iye yekha, "Nditangokhudza kasonga ka mkanjo wake, ine ndidzachiritsidwa."

22 Ndipo Yesu anatembenuka namuona mayiyo nati, "Limbani mtima mayi iwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa." Nthawi yomweyo mayiyo anachiritsidwa.

23 Yesu atalowa mʼnyumba ya mkulu wa sunagoge ndi kuona oyimba zitoliro ndi gulu la anthu ochita phokoso, 24 anati, "Tulukani, mtsikanayu sanafe koma ali mtulo." Koma anamuseka Iye. 25 Atangowatulutsa anthuwo, analowa mʼnyumba ndipo anagwira dzanja la mtsikanayo ndipo anauka. 26 Mbiriyi inamveka mʼdera lonse.

Veja também