2 Amuna ena anabwera ndi munthu wakufa ziwalo kwa Iye atamugoneka pa mphasa. Yesu ataona chikhulupiriro chawo anati kwa wakufa ziwaloyo, "Limba mtima mwana wanga, machimo ako akhululukidwa."
3 Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, "Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano."
4 Ndipo podziwa maganizo awo Yesu anati, "Bwanji mukuganiza zoyipa mʼmitima mwanu? 5 Chapafupi ndi chiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ kapena kunena kuti, ‘Imirira ndipo yenda?’ 6 Tsono kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko wokhululuka machimo, pamenepo anati kwa wakufa ziwaloyo, ‘Imirira, tenga mphasa yako kazipita kwanu.’ " 7 Ndipo munthuyo anayimirira napita kwawo.