Yesu Achiritsa Osaona ndi Osayankhula
27 Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, "Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!"
28 Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti, "Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?"
Iwo anayankha kuti, "Inde Ambuye."
29 Pomwepo anakhudza maso awo nati, "Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu." 30 Ndipo anayamba kuona. Yesu anawachenjeza kwambiri nati, "Onani, wina aliyense asadziwe za zimenezi." 31 Koma iwo anatuluka mʼnyumbamo nafalitsa za Iye mʼchigawo chonse.