10 Yehova anawuza Mose kuti, 11 "Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni wabweza mkwiyo wanga pa Aisraeli chifukwa sanalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine ndekha. Nʼchifukwa chake sindinawawononge mu mkwiyo wanga. 12 Tsono muwuze kuti ndikhazikitsa pangano langa la mtendere ndi iye. 13 Ndikupangana naye pangano la unsembe wosatha, iyeyo pamodzi ndi zidzukulu zake zonse, chifukwa sanalole kuti anthu awukire Ine Mulungu, ndipo anachita ntchito yopepesera machimo Aisraeli."
Publicidade
Publicidade