Pular para o conteúdo
Publicidade

Provérbios 4

Nzeru Iposa Zonse

1 Ananu, mverani malangizo a abambo anu;

tcherani khutu kuti mupeze nzeru zodziwira zinthu.

2 Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino.

Choncho musasiye malangizo anga.

3 Paja ndinalinso mwana mʼnyumba mwa abambo anga;

mwana mmodzi yekha wapamtima pa amayi anga.

4 Ndipo abambo anandiphunzitsa ndi mawu akuti,

"Ugwiritse mawu anga pa mtima pako,

usunge malamulo anga kuti ukhale ndi moyo.

5 Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu;

usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.

6 Usasiye nzeru ndipo idzakusunga.

Uziyikonda ndipo idzakuteteza.

Veja também