Pular para o conteúdo
Publicidade

MIYAMBO 5

8 Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo,

usayandikire khomo la nyumba yake,

9 kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena;

ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,

10 kapenanso alendo angadyerere chuma chako

ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.

11 Potsiriza pa moyo wako udzabuwula,

thupi lako lonse litatheratu.

12 Ndipo udzati, "Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo!

Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!

13 Sindinamvere aphunzitsi anga

kapena alangizi anga.

14 Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke

pakati pa msonkhano wonse."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também